John 11:55 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chikondwerero cha Paska chija chinkayandikira. Choncho anthu ambiri ochokera ku midzi adapita ku Yerusalemu kukachita mwambo wa kudziyeretsa, Paska isanayambe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka ku milaga, usanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ya Paska wa Ayuda itayandikira, ambiri anakwera kupita ku Yerusalemu kuchokera ku madera a ku midzi chifukwa cha mwambo wa kuyeretsedwa Paska asanafike.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Paskha wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kucoka ku miraga, usanafike Paskha, kukadziyeretsa iwo okha.