John 11:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ophunzira akewo adati, “Aphunzitsi, tsopano apa Ayuda ankafuna kukuponyani miyala, ndiye mukuti mupitenso komweko?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ophunzira ananena ndi Iye, Rabi, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ophunzira akewo anati, “Rabi, posachedwa pomwepa Ayuda anafuna kukugendani ndi miyala, koma Inu mukupitanso komweko?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akuphunzira ananena ndi iye, Ambuye, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi?