John 12:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi imeneyo ophunzira ake sadazimvetse zimenezo. Koma Yesu atauka ndi ulemerero, iwo adakumbukira kuti zimenezi zidalembedwa kunena za Iye, ndipo kuti adamchitiradi zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Izi sanazidziwa ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Poyamba ophunzira ake sanamvetsetse zonsezi. Koma pomwe Yesu analemekezedwa ndi pamene anazindikira kuti zinthu izi zinalembedwa ndipo kuti anamuchitira Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Izisanazidziwa aku phunzira ace poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukila kuti izi zinalembedwa za iye, ndi kuti adamcitira iye izi.