John 12:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja pamene Yesu adaaitana Lazaro kuti atuluke m'manda nkumuukitsa kwa akufa, panali anthu ambirimbiri. Tsono iwowo ankasimba m'mene adaaziwonera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo khamulo limene linali pamodzi ndi Iye, m'mene anaitana Lazaro kutuluka kumanda, namuukitsa kwa akufa, anachita umboni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano gulu la anthu lomwe linali naye pa nthawi imene amaukitsidwa Lazaro ku manda linapitiriza kuchitira umboni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo khamulo limene linali pamodzi ndi iye, m'mene anaitana Lazaro kuturuka kumanda, namuukitsa kwa akufa, anacita umboni.