John 12:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena zoona, mbeu ya tirigu imakhalabe imodzi yomweyo ngati siigwa m'nthaka nkufa. Koma ikafa, imabala zipatso zambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti, ‘Mbewu ya tirigu imakhala imodzi yokha ngati sikugwa mʼnthaka ndi kufa. Koma ngati imfa, imabereka mbewu zambiri.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala cipatso cambiri.