John 12:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati munthu anditumikira Ine, anditsatire, motero kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Munthu akanditumikira Ine, Atate anga adzamlemekeza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga, Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamcitira ulemu iyeyu,