John 12:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panali khamu la anthu pamenepo. Tsono pamene adamva mauwo, adati, “Kwagunda bingu.” Koma ena adati, “Mngelo walankhula naye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gulu la anthu lomwe linali pamenepo litamva linati, “Kwagunda bingu,” ena anati, “Mngelo wayankhula kwa Iye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi iye.