John 12:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aja adamuuza kuti, “Ife tidaŵerenga m'Malamulo mwathu kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Nanga Inu mukuneneranji kuti Mwana wa Munthu ayenera kupachikidwa? Mwana wa Munthuyo ndani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo khamulo linayankha Iye, Tidamva ife m'chilamulo kuti Khristu akhala kunthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa Munthu amene ndani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gulu la anthu linayankha kuti, “Ife tinamva kuchokera mʼmalamulo kuti Khristu adzakhala kwamuyaya, nanga bwanji Inu mukunena kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa?’ Kodi Mwana wa Munthuyu ndani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo khamulo linayankha iye, Tidamva ife m'cilamulo kuti Kristu akhala ku nthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa munthu amene ndani?