John 12:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mulungu adadetsa maso ao, ndipo adabunthitsa nzeru zao, kuti maso ao asaone, nzeru zao zisamvetse, kuti angatembenuke mtima, ndipo Ine ndingaŵachiritse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao; kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo ndingawachiritse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iye wachititsa khungu maso awo ndi kuwumitsa mitima yawo, kotero kuti iwo sangathe kuona ndi maso awo, kapena kuzindikira ndi mitima yawo, kapena kutembenuka kuti Ine ndikanawachiza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
4 Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao; Kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima, Nangatembenuke, Ndipo ndingawaciritse.