John 12:48 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu amene akana Ine, ndipo salandira mau anga, alipo amene adzamuweruze. Adzazengedwa mlandu pa tsiku lomaliza chifukwa cha mau omwe ndakhala ndikulankhulaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye, mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomaliza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
12 iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye; 13 mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomariza.