John 12:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaatero osati chifukwa chodera nkhaŵa osaukawo, koma chifukwa anali mbala. Iye ankasunga thumba la ndalama, nkumabamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ananena ichi si chifukwa analikusamalira osauka, koma chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye sananene izi chifukwa cha kuganizira osauka koma chifukwa anali mbava; ngati wosunga thumba la ndalama, amabamo zomwe ankayikamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ananena ici si cifukwa analikusamalira osauka, koma cifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amabazoikidwamo.