John 13:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu atatsuka mapazi a ophunzira ake, adavalanso mwinjiro wake nakakhalanso podyera paja. Kenaka adaŵafunsa kuti, “Kodi mwazimvetsa zimene ndakuchitiranizi?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo, atatha Iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ake, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye atamaliza kusambitsa mapazi awo anavala zovala zake ndi kubwerera pamalo pake. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukuzindikira zimene ndakuchitirani inu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo, atatha iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ace, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga cimene ndakucitirani inu; mucizindikira kodi?