John 13:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mauŵa sindikunenera nonsenu ai. Ndikuŵadziŵa amene ndaŵasankha. Koma ziyenera kuchitikadi zimene Malembo adanena kuti, ‘Amene ankadya nane pamodzi, yemweyo ndiye adandiwukira.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine sindikunena za inu nonse. Ine ndikudziwa amene ndinawasankha. Koma izi zikukwaniritsa malemba: ‘Iye amene akudya nawo chakudya changa, ndiye amene anandiwukira.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti colemba cikwaniridwe, iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine cinendene cace.