John 13:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatero adathira madzi m'beseni, nayamba kutsuka mapazi a ophunzira ake, nkumaŵapukuta ndi nsalu yopukutira ija imene adaaimanga m'chiwuno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo anathira madzi m'nsambidwe, nayamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira, chimene anadzimanga nacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atachita izi, anathira madzi mʼbeseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira chimene anachimanga mʼchiwuno mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo anathira madzi m'nsambidwe, nayamba kusambitsa mapazi a akuphunzira ace, ndi kuwapukuta ndi copukutira, cimene anadzimanga naco,