John 14:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita Ine kwa Atate.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene akhulupirira Ine adzachita zimene Ine ndakhala ndikuchita. Iye adzachita ngakhale zinthu zazikulu kuposa zimenezi, chifukwa ndikupita kwa Atate.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, nchito zimene ndicita Ine adzazicitanso iyeyu; ndipo adzacita zoposa izi; cifukwa ndipita Ine kwa Atate.