John 14:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiye Mzimu wa choonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona Iye, kapena kumzindikira Iye. Inu mumzindikira Iye; chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nkhosweyo ndiye Mzimu wachoonadi. Dziko lapansi silingalandire Nkhosweyi chifukwa samuona kapena kumudziwa. Koma inu mumamudziwa pakuti amakhala nanu ndipo adzakhala mwa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndiye Mzimu wa coonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; cifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.