John 14:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yudasi, si Iskariote, ananena ndi Iye, Ambuye, chachitika chiyani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yudasi (osati Yudasi Isikarioti) anati, “Koma Ambuye, nʼchifukwa chiyani mukufuna kudzionetsa nokha kwa ife, osati ku dziko lapansi?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yudase, si Isikariote, ananena ndi iye, Ambuye, cacitika ciani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi?