John 15:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukadakhala a mkhalidwe wao, akadakukondani chifukwa cha kukhala anzao. Koma amadana nanu, chifukwa Ine ndidakusankhani pakati pa iwo, motero sindinu anzao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mukanakhala anthu a dziko lapansi, dziko lapansi likanakukondani ngati anthu ake omwe. Koma mmene zilili, inu si anthu a dziko lapansi. Ine ndakusankhani kuchokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake dziko lapansi limakudani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zace za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, cifukwa ca ici likudani inu.