John 15:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumbukirani mau aja amene ndidakuuzani kuti, ‘Wantchito saposa mbuye wake.’ Ngati Ine adandisautsa, inunso adzakusautsani. Ngati adamvera mau anga, adzamvera mau anunso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kumbukirani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumbukirani mawu amene ndinayankhula nanu akuti, ‘Palibe wantchito amene amaposa bwana wake.’ Ngati anandizunza Ine, iwo adzakuzunzaninso inu. Ngati anamvera chiphunzitso changa, iwo adzamvera chanunso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kumbukilani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkuru ndi mbuye wace. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulonda-londani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.