John 15:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khalani mwa Ine, ndipo Inenso ndidzakhala mwa inu. Nthambi siingathe kubala zipatso payokha ngati siikhala pa mtengo wake. Momwemonso inu ngati simukhala mwa Ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala cipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine.