John 16:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa coonadi, adzatsogolera inu m'coonadi conse; pakuti sadzalankhula za iye mwini; koma zinthu ziri zonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zirinkudza adzakulalikirani.