John 16:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ophunzira ake ena adayamba kufunsana kuti, “Kodi nchiyani akutiwuzachi? Akuti, ‘Kanthaŵi pang'ono ndipo simudzandiwonanso, koma patapitanso kanthaŵi pang'ono, mudzandiwona.’ Akutinso, ‘Chifukwa ndikupita kwa Atate.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa ophunzira ake tsono anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chimene anena ndi ife, Kanthawi ndipo simundiona; ndiponso kanthawi, ndipo mudzandiona; ndipo, chifukwa ndimuka kwa Atate?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena a ophunzira ake anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi Iye akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso,’ ndi ‘ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso,’ ndiponso ‘chifukwa ndikupita kwa Atate?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa akuphunzira ace tsono anati wina ndi mnzace, ici nciani cimene anena ndi ife, Kanthawi ndipo simundiona; ndiponso kanthawi, ndipo mudzandiona; ndipo, cifukwa ndimuka kwa Atate?