John 16:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi yochira mai amavutika chifukwa nthaŵi yake yafika. Koma pamene wabadwa mwana, saganizakonso za kuzunzikako, chifukwa cha chimwemwe chakuti kunja kuno kwabadwa mwana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mkazi pamene akuti abale ali nacho chisoni, chifukwa yafika nthawi yake; koma pamene wabala mwana, sakumbukiranso kusaukako, chifukwa cha chimwemwe kuti wabadwa munthu kudziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mkazi pamene akuti abale ali naco cisoni, cifukwa yafika nthawi yace; koma pamene wabala mwana, sakumbukilanso kusaukako, cifukwa ca cimwemwe kuti wabadwa munthu ku dziko lapansi.