John 16:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano tadziŵa kuti mumadziŵa zonse, ndipo palibenso chifukwa choti munthu akufunseni mafunso. Nchifukwa chake tikukhulupirira kuti ndinu ochokera kwa Mulungu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsopano tidziwa kuti mudziwa zonse, ndipo mulibe kusowa kuti wina akafunse Inu; mwa ichi tikhulupirira kuti munatuluka kwa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano ife tikuona kuti Inu mumadziwa zinthu zonse ndi kuti sipafunika wina aliyense kukufunsani. Mwa ichi ife takhulupirira kuti Inu munachokera kwa Mulungu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsopano tidziwa kuti mudziwa zonse, ndipo mulibe kusowa kuti wina akafunse Inu; mwa ici tikhulupirira kuti munaturuka kwa Mulungu.