John 16:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ndimati muzimve zimenezi kuti nthaŵi yakeyo ikadzafika, mudzakumbukire kuti ndidaakuuziranitu.” “Sindidakuuzeni zimenezi poyamba paja ai, chifukwa ndinali nanu pamodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanena kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndakuwuzani izi kuti nthawi ikadzafika mudzakumbukire kuti Ine ndinakuchenjezani kale. Ine sindinakuwuzeni izi poyamba paja chifukwa ndinali nanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanena kwa inu kuyambira paciyambi, cifukwa ndinali pamodzi ndi inu.