John 16:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe ndikukuuzani zoona, kuti nkwabwino koposa kwa inu kuti ndichoke. Pakuti ngati sindichoka, Nkhoswe ija siidzabwera kwa inu. Koma ngati ndipita, ndidzaitumiza kwa inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinena Ine choonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu ndakuwuzani zoona. Ine ndikuti kuli bwino kwa inu kuti ndichoke. Ngati sindichoka, Nkhosweyo sidzabwera kwa inu, koma ngati Ine ndipita, ndidzamutumiza kwa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinena Ine coonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndicoke Ine; pakuti ngati sindicoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma iye kwa inu.