John 17:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndaŵaphunzitsa mau anu. Anthu odalira zapansipano amadana nawo, chifukwa iwo sali anzao, monga Inenso sindili mnzao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi, linadana nao, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi linadana nao, cifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.