John 17:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti ndaŵapatsa mau amene mudandiwuza Ine, ndipo aŵalandira. Akudziŵadi kuti ndidachokera kwa Inu, ndipo sakayika kuti ndinu mudandituma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinatuluka kwa Inu, ndipo anakhulupirira kuti Inu munandituma Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinaturuka kwa Inu, ndipo anakhulupira kuti Inu munandituma Ine.