John 18:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simoni Petro anali ndi lupanga. Adalisolola, natema kapolo wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu la ku dzanja lamanja. Kapoloyo dzina lake anali Malkusi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, analisolola nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namsenga khutu lake lamanja. Koma dzina lake la kapoloyo ndiye Malkusi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Simoni amene anali ndi lupanga analitulutsa ndi kutema nalo wantchito wa wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake la kudzanja lamanja. (Dzina la wantchitoyo ndi Makusi).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, analisolola nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namsenga khutu lace lamanja. Koma dzina lace la kapoloyo ndiye Malko.