John 18:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Antchito pamodzi ndi asilikali achiyuda aja adaaimirira pamenepo atasonkha moto nkumaotha, chifukwa kunkazizira. Petro nayenso adaaimirira pomwepo nkumaotha nao motowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma akapolo anyamata analikuimirirako, atasonkha moto wamakala; pakuti kunali kuzizira; ndipo analikuotha moto; koma Petronso anali nao alikuimirira ndi kuotha moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza kunkazizira, anyamata antchito ndi akuluakulu ena anasonkha moto wamakala namawotha atayimirira mozungulira. Petro nayenso anayimirira pamodzi ndi iwo namawotha nawo motowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma akapolo ndi anyamata analikuimirirako, atasonkha mota wamakara; pakuti kunali kuzizira; ndipo analikuotha moto; koma Petronso anali nao alikuimirira ndi kuotha moto.