John 18:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simoni Petro anali chililibe akuwotha nao moto. Tsono ena adamufunsa kuti, “Kodi iwenso sindiwe mmodzi mwa ophunzira a munthu uja?” Petro adakana, adati, “Iyai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Simoni Petro analikuimirira ndi kuotha moto. Pomwepo anati kwa iye, Suli iwenso wa ophunzira ake kodi? Iyeyu anakana, nati, Sindine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Simoni Petro anali chiyimirire kuwotha moto, anafunsidwa kuti, “Kodi iwe si mmodzi wa ophunzira ake?” Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Simoni Petro analikuimirira ndi kuotha moto. Pomwepo anati kwa iye, Suli iwenso wa akuphunzira ace kodi? Iyeyu anakana, nati, Sindine.