John 18:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yudasiyo adatenga gulu la asilikali achiroma pamodzi ndi asilikali a ku Nyumba ya Mulungu amene akulu a ansembe ndi Afarisi adaaŵatuma. Iwo adapita kumundako atatenga nyale ndi miyuni ndi zida zankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yudasi, m'mene adatenga gulu la asilikali ndi anyamata, kwa ansembe aakulu ndi Afarisi, anadza komweko ndi nyali ndi miuni ndi zida.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yudasi anabwera ku munda, akutsogolera gulu la asilikali ndi akuluakulu ena ochokera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi. Iwo anali atanyamula miyuni, nyale ndi zida.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yudase, m'mene adatenga gulu la asilikari ndi anyamata, kwa ansembe akulu ndi Afarisi, anadza komweko ndi nyali ndi miuni ndi zida.