John 18:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pilato adati, “Ine ndine Myuda kodi? Anthu a mtundu wako womwe ndiponso akulu a ansembe ndiwo akupereka kwa ine. Udachita chiyani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pilato anayankha, Ndili ine Myuda kodi? Mtundu wako ndi ansembe aakulu anakupereka kwa ine; wachita chiyani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pilato anayankha kuti, “Kodi iwe ukuganiza kuti ine ndine Myuda? Ndi anthu ako ndi akulu a ansembe ako amene akupereka iwe kwa ine. Kodi walakwanji?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pilato anayankha, ndiri ine Myuda kodi? Mtundu wako ndi ansembe akulu anakupereka kwa ine; wacita ciani?