John 19:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Pilato adamufunsa kuti, “Sukundiyankha? Kodi sukudziŵa kuti ine ndili ndi mphamvu zokumasula, ndiponso mphamvu zokupachika?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Pilato ananena kwa Iye, Simulankhula ndi ine kodi? Simudziwa kodi kuti ulamuliro ndili nao wakukumasulani, ndipo ndili nao ulamuliro wakukupachikani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pilato anati, “Kodi ukukana kundiyankhula ine? Kodi sukuzindikira kuti ine ndili ndi mphamvu yokumasula ndiponso mphamvu yokupachika?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Pilato ananena kwa iye, Simulankhula ndi ine kodi? simudziwa kodi kuti ulamuliro ndiri nao wakukumasulani, ndipo ndiri nao ulamuliro wakukupacikani?