John 19:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamva mau ameneŵa, Pilato adafuna ndithu kummasula Yesu. Koma Ayuda adafuula kuti, “Mukammasula ameneyu, sindinu bwenzi la Mfumu ya ku Roma. Aliyense wodziyesa mfumu, ngwoukira Mfumu ya ku Romayo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pa ichi Pilato anafuna kumasula Iye; koma Ayuda anafuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyambira pamenepo Pilato anayesa kuti amumasule Yesu, koma Ayuda anapitirira kufuwula kuti, “Ngati mumumasula munthuyu kuti apite, inu si bwenzi la Kaisara.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pa ici Pilato anafuna kumasula iye; koma Ayuda anapfuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.