John 19:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pilato atamva zimenezo, adatulutsa Yesu, nakakhala pa mpando woweruzira milandu, pa malo otchedwa “Bwalo lamiyala” (pa Chiyuda amati “Gabata.”)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anatuluka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lake, Bwalo lamiyala, koma m'Chihebri, Gabata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pilato atamva zimenezi, iye anamutulutsa Yesu kunja ndi kukhala pansi pa mpando wa woweruza pamalo otchedwa Mwala Wowaka (umene pa Chiaramaiki ndi Gabata).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anaturuka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lace; Bwalo lamiyala, koma m'Cihebri, Gabata,