John 19:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iwo adafuula kuti, “Mchotseni! Mchotseni! Kampachikeni pa mtanda!” Pilato adaŵafunsa kuti, “Ndipachike Mfumu yanu kodi?” Akulu a ansembe adati, “Tilibe mfumu ina ai, koma Mfumu ya ku Roma yokha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anafuula iwowa, Chotsani, Chotsani, mpachikeni Iye! Pilato ananena nao, Ndipachike mfumu yanu kodi? Ansembe aakulu anayankha, Tilibe mfumu koma Kaisara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwo anafuwula kuti, “Choka nayeni! Choka nayeni! Mpachikeni!” Pilato anafunsa kuti, “Kodi ine ndipachike mfumu yanuyi?” Akulu a ansembe anayankha kuti, “Ife tilibe mfumu ina koma Kaisara.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anapfuula iwowa, Cotsani, Cotsani, mpacikeni iye! Pilato ananena nao, Ndipacike Mfumu yanu kodi? Ansembe akulu anayankha, Tiribe Mfumu koma Kaisara.