John 19:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ayuda ambiri adachiŵerenga chidziŵitsocho, chifukwa pamalo pamene Yesu adaapachikidwapo panali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Chidziŵitsocho chidalembedwa m'chilankhulo cha Ayuda, cha Aroma, ndiponso cha Agriki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; chifukwa malo amene Yesu anapachikidwapo anali pafupi pa mudziwo; ndipo linalembedwa m'Chihebri, ndi m'Chilatini, ndi m'Chigriki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayuda ambiri anawerenga chikwangwanichi, pakuti pamalo pamene Yesu anapachikidwapo panali pafupi ndi mzinda ndipo chikwangwanicho chinalembedwa mu Chiaramaiki, Chilatini ndi Chigriki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; cifukwa malo amene Yesu anapaeikidwapo anali pafupipa mudziwo; ndipo linalembedwa m'Cihebri, ndi m'Ciroma, ndi m'Cihelene.