John 19:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono asilikaliwo adauzana kuti, “Tisaung'ambe, koma tichite mayere kuti tiwone ukhala wa yani.” Zidaayenda choncho kuti zipherezere zimene Malembo adanena kuti, “Adagaŵana zovala zanga, ndipo mkanjo wanga adauchitira mayere.” Zimenezi adachitadi asilikali aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake anati wina kwa mnzake, Tisang'ambe awa, koma tichite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zovala zanga mwa iwo okha, ndi pa malaya anga anachitira maere. Ndipo asilikali anachita izi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni tisachingʼambe koma tichite maere kuti tione amene achitenge.” Izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe amene anati, “Iwo anagawana zovala zanga pakati pawo ndi kuchita maere pa zovala zangazo.” Choncho izi ndi zimene asilikali anachita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace anati wina kwa mnzace, Tisang'ambe awa, koma ticite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zobvala zanga mwa iwo okha, ndi pa maraya anga anacitira maere. Ndipo asilikari anacita izi.