John 19:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Linali tsiku lokonzekera chikondwerero cha Paska. Akulu a Ayuda sadafune kuti mitemboyo ikhalebe pa mtanda pa tsiku la Sabata, chifukwa Lasabata limenelo linali lalikulu. Nchifukwa chake adakapempha Pilato kuti alamule kuti akathyole miyendo ya anthu opachikidwa aja, nkuŵachotsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Ayuda, popeza panali tsiku lokonzera, kuti mitembo ingatsale pamtanda tsiku la Sabata, pakuti tsiku lomwelo la Sabata linali lalikulu, anapempha Pilato kuti miyendo yao ithyoledwe, ndipo achotsedwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza linali Tsiku Lokonzekera ndipo tsiku linalo linali Sabata lapadera; Ayuda sanafune kuti mitembo ikhale pa mtanda pa Sabata, iwo anapempha Pilato kuti akathyole miyendo ndi kutsitsa mitemboyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Ayuda, popeza panali tsiku lokonzera, kuti 1 mitembo ingatsale pamtanda tsiku la Sabata, pakuti tsiku lomwelo la Sabata linali lalikuru, anapempha Pilato kuti miyendo yao ityoledwe, ndipo acotsedwe.