John 19:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono asilikali adabwera, nathyola miyendo ya mmodzi mwa aŵiri aja amene adaapachikidwa pamodzi ndi Yesu. Adateronso ndi mnzake uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake anadza asilikali nathyola miyendo ya woyambayo, ndi ya winayo wopachikidwa pamodzi ndi Iye;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chake asilikali anabwera ndi kuthyola miyendo ya munthu oyamba amene anapachikidwa ndi Yesu ndipo kenaka ya winayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace anadza asilikari natyola miyendo ya woyambayo, ndi ya winayo wopacikidwa pamodzi ndi iye;