John 19:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Yosefe wa ku Arimatea adapempha Pilato kuti amlole kukachotsa mtembo wa Yesu. (Yosefeyo anali wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa choopa akulu a Ayuda.) Tsono Pilato atamlola, iye adakachotsa mtembowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chitatha ichi Yosefe wa ku Arimatea, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa cha kuopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akachotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato analola. Chifukwa chake anadza, nachotsa mtembo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka, Yosefe wa ku Arimateyu anakapempha mtembo wa Yesu kwa Pilato. Tsono Yosefe anali wophunzira wa Yesu koma mobisa chifukwa iye ankaopa Ayuda. Atalandira chilolezo kwa Pilato, anakatsitsa mtembo wa Yesu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
6 Citatha ici. Y osefe wa ku Arimateya, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, cifukwa ca kuopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akacotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato analola. Cifukwa cace anadza, nacotsa mtembo wace.