John 19:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pilato adatulukanso nauza Ayudawo kuti, “Onani, ndikumtulutsira kuli inu kuno kuti mudziŵe kuti sindikumpeza chifukwa chilichonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Pilato anatulukanso kunja, nanena nao, Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa Iye chifukwa chilichonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pilato anatulukanso ndipo anati kwa Ayuda, “Taonani, ine ndikumubweretsa kuti inu mudziwe kuti ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Pilato anaturukanso kunja, nanena nao, Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa iye cifukwa ciri conse.