John 19:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aŵiriwo adatenga mtembo wa Yesu, naukulunga m'nsalu zoyera zabafuta pamodzi ndi zonunkhira zija, potsata mwambo wamaliro wachiyuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu nawukulunga pamodzi ndi zonunkhiritsa mu nsalu za mtundu woyera monga mwa mwambo wa maliro wa Ayuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsaru zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.