John 19:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumene Yesu adaapachikidwako kunali munda. Ndipo m'mundamo munali manda atsopano, amene anali asanaikemo munthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kunali munda kumalo kumene anapachikidwako, ndi m'mundamo munali manda atsopano m'mene sanaikidwamo munthu aliyense nthawi zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamalo pamene anapachikidwa Yesu panali munda ndipo mʼmundamo munali manda atsopano mʼmene munali simunayikidwemo aliyense.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kunali munda kumalo kumene anapacikidwako, ndi m'mundamo munali manda atsopano m'mene sanaikidwamo munthu ali yense nthawi zonse.