John 19:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akulu a ansembe ndi asilikali a ku Nyumba ya Mulungu aja ataona Yesu, adafuula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” Pilato adaŵauza kuti, “Mtengeni inuyo mukampachike, ine ndiye sindikumpeza chifukwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene ansembe aakulu ndi anyamata anamuona Iye, anafuula nanena, Mpachikeni, mpachikeni. Pilato ananenana nao, Mtengeni Iye inu nimumpachike; pakuti ine sindipeza chifukwa mwa Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atangomuona Iye akulu a ansembe ndi akuluakulu ena anafuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” Koma Pilato anayankha kuti, “Inu mutengeni ndi kumupachika. Koma ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene ansembe akulu ndi anyamata anamuona iye, anapfuula nanena, Mpacikeni, mpacikeni, Pilato ananena nao, Mtengeni iye inu nimumpaeike; pakuti ine sindipeza cifukwa mwa: iye.