John 2:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yesu adapanga mkwapulo wazingwe nayamba kuŵatulutsira onse kunja, pamodzi ndi nkhosa ndi ng'ombe zao zomwe. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama aja, naŵamwazira ndalama zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, anatulutsa onse m'Kachisimo, ndi nkhosa ndi ng'ombe; nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagubuduza magome;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, anaturutsa onse m'Kacisimo, ndi nkhosa ndi ng'ombe; nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagubuduza magome;