John 2:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu anali m'Yerusalemu pa chikondwerero cha Paska, anthu ambiri adayamba kuika chikhulupiriro chao pa Iye, poona zozizwitsa zimene ankachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene anali m'Yerusalemu pa Paska pachikondwerero, ambiri anakhulupirira dzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene anachitazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano Iye ali mu Yerusalemu pa phwando la Paska, anthu ambiri anaona zizindikiro zodabwitsa zimene amachita ndipo anakhulupirira dzina lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene anali m'Yerusalemu pa Paskha paphwando, ambiri anakhulupirira dzinalace, pakuona zizindikilo zace zimene anaeitazi.