John 2:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sankalira kuti wina achite chomuuza za munthu aliyense. Pakuti mwiniwakeyo ankadziŵa za m'mitima mwa anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo sanasowe wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye sanafune umboni wa wina aliyense popeza amadziwa zomwe zinali mʼmitima mwa anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo sanasowa wina acite umboni za munthu; pakuti anadziwa iye yekha cimene cinali mwa munthu.