John 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo panali mbiya zamwala zisanu ndi imodzi, zimene adaaziikapo chifukwa cha mwambo wa kudziyeretsa wa Ayuda. M'mbiya iliyonse munkaloŵa madzi okwanira malita zana limodzi kapena kupitirirapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipopanali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.